Ndipo ukaike guwa la nsembe lofukizapo lagolide chakuno cha likasa la mboni, numange pa chihema nsalu yotsekera pakhomo.
Eksodo 40:26 - Buku Lopatulika Ndipo anaika guwa la nsembe lagolide m'chihema chokomanako chakuno cha nsalu yotchinga; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaika guwa la nsembe lagolide m'chihema chokomanako chakuno cha nsalu yotchinga; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'chihema chamsonkhanomo adaikamo guwa lagolide patsogolo pa nsalu yochinga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anayika guwa la golide mu tenti ya msonkhano patsogolo pa katani |
Ndipo ukaike guwa la nsembe lofukizapo lagolide chakuno cha likasa la mboni, numange pa chihema nsalu yotsekera pakhomo.
ndipo wansembeyo aviike chala chake m'mwazimo, nawaze mwaziwo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova chakuno cha nsalu yotchinga, ya malo opatulika.
Inu akhungu, pakuti choposa nchiti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo?
Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma chifukwa cha khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ichi, kuti akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.
Pakuti chilamulo, pokhala nao mthunzi wa zokoma zilinkudza, osati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo, sichikhozatu, ndi nsembe zomwezi chaka ndi chaka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira.
kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.
Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Khristu wolungama;