Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 23:19 - Buku Lopatulika

19 Inu akhungu, pakuti choposa nchiti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Inu akhungu, pakuti choposa nchiti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Anthu akhungu inu! Chachikulu nchiti, choperekedwa chija, kapena guwa lansembe lija limene likusandutsa choperekedwacho kuti chikhale chopatulika?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Inu anthu akhungu! Chopambana nʼchiyani: mphatso, kapena guwa limene limayeretsa mphatsoyo?

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 23:19
6 Mawu Ofanana  

Uchitire guwa la nsembe choteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo guwa la nsembelo likhale lopatulika kwambiri; chilichonse chikhudza guwa la nsembelo chikhale chopatulika.


Ndipo uzipatule, kuti zikhale zopatulika ndithu; zonse zakuzikhudza zidzakhala zopatulika.


Munthu akanyamulira nyama yopatulika m'ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya chilichonse, ndi ngudulira, kodi chisandulika chopatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai.


Inu opusa, ndi akhungu: pakuti choposa nchiti, golide kodi, kapena Kachisi amene ayeretsa golideyo?


Ndiponso, Amene aliyense akalumbira kutchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula mtulo wa pamwamba pake wadzimangirira.


Chifukwa chake wakulumbira kutchula guwa la nsembe, alumbira limenelo ndi zonse za pamwamba pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa