Eksodo 40:17 - Buku Lopatulika Ndipo kunali, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa chihema, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa Kachisi, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero pa tsiku loyamba la mwezi woyamba chaka chachiŵiri, malo opatulika adautsidwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero anayimika chihema tsiku loyamba la mwezi woyamba mʼchaka chachiwiri. |
ndipo Mose anautsa chihema, nakhazika makamwa ake, naimika matabwa ake, namangapo mitanda yake, nautsa mizati ndi nsanamira zake.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, m'chihema chokomanako, tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
Ndipo kunachitika, chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la makumi awiri la mweziwo, kuti mtambo unakwera kuchokera kwa chihema cha mboni.
Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kuutsa chihema, nachidzoza ndi kuchipatula, ndi zipangizo zake zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, nazidzoza ndi kuzipatula;
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
Ndipo tsiku loutsa Kachisi mtambo unaphimba Kachisi, ndiwo chihema chokomanako; ndicho chihema chaumboni, ndipo madzulo padaoneka pa Kachisi ngati moto, kufikira m'mawa.