Pamene Farao anachimva ichi, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m'dziko la Midiyani; nakhala pansi pachitsime.
Eksodo 4:19 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena ndi Mose mu Midiyani, Muka, bwerera kunka ku Ejipito; pakuti adafa anthu onse amene anafuna moyo wako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'Midiyani, Muka, bwerera kunka ku Ejipito; pakuti adafa anthu onse amene anafuna moyo wako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauza Mose ku Midiyani kuja kuti, “Bwerera ku Ejipito tsopano popeza kuti onse aja ankafuna kukuphaŵa adamwalira.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawiyi Yehova anali atamuwuza kale Mose ku Midiyani kuti, “Bwerera ku Igupto, pakuti anthu onse amene amafuna kukupha aja anamwalira.” |
Pamene Farao anachimva ichi, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m'dziko la Midiyani; nakhala pansi pachitsime.
Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.
nati, Tauka, nutenge kamwana ndi amake, nupite kudziko la Israele: chifukwa anafa uja wofuna moyo wake wa kamwanako.