Eksodo 39:6 - Buku Lopatulika Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolide, yolocha ngati malochedwe a chosindikizira, ndi maina a ana a Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolide, yolocha ngati malochedwe a chosindikizira, ndi maina a ana a Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka adakonza miyala yakongola ya mtundu wa onikisi, naikhazika m'zoikamo zake zagolide. Tsono adaizokota monga amachitira pa chidindo, nalembapo mozokota bwino maina onse a ana aamuna a Israele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anakonza miyala ya onikisi ndi kuyiika mu zoyikamo zake zagolide ndipo anazokota mayina a ana a Israeli monga amachitira pa chidindo. |
Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.
Ndipo uiike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Israele; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ake awiri, akhale chikumbutso pamaso pa Yehova.
Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nao unali woombera kumodzi wa chiombedwe chomwechi; wa golide, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adauza Mose.
Unali mu Edeni, munda wa Mulungu, mwala uliwonse wa mtengo wake unali chofunda chako, sardiyo, topazi, diamondi, berulo, sohamu, ndi yaspi, safiro, nofeki, bareketi, ndi golide; malingaka ako ndi akazi ako anakutumikira tsiku lolengedwa iwe zinakonzekeratu.