Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 39:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iwo anakonza miyala ya onikisi ndi kuyiika mu zoyikamo zake zagolide ndipo anazokota mayina a ana a Israeli monga amachitira pa chidindo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolide, yolocha ngati malochedwe a chosindikizira, ndi maina a ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolide, yolocha ngati malochedwe a chosindikizira, ndi maina a ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Kenaka adakonza miyala yakongola ya mtundu wa onikisi, naikhazika m'zoikamo zake zagolide. Tsono adaizokota monga amachitira pa chidindo, nalembapo mozokota bwino maina onse a ana aamuna a Israele.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 39:6
8 Mawu Ofanana  

Nzeru singagulidwe ndi golide wa ku Ofiri, kapena ndi miyala ya onikisi kapena ya safiro.


miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa efodi ndi pa chovala cha pachifuwa.


Mayina a ana a Israeli uwazokote pa miyala iwiriyo, monga momwe amachitira mmisiri wozokota miyala. Ndipo uyike miyalayo mu zoyikamo zake zagolide.


Umangirire miyala iwiriyi pa tinsalu ta mʼmapewa ta efodi tija ngati miyala ya chikumbutso cha ana a Israeli. Aaroni azinyamula mayinawo mʼmapewa ake kuti akhale chikumbutso pamaso pa Yehova.


“Utenge miyala iwiri ya onikisi ndipo uzokotepo mayina a ana a Israeli.


miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa Efodi ndi pa chovala cha pachifuwa.


Lamba womangira efodi anali wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Anali nsalu imodzi ndi efodiyo, wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala, monga momwe Yehova analamulira Mose.


Iwe unkakhala ngati mu Edeni, munda wa Mulungu. Miyala yokongola ya mitundu yonse: rubi, topazi ndi dayimondi, kirisoliti, onikisi, yasipa, safiro, kalineliyoni ndi berili ndiwo inali zofunda zako. Ndipo zoyikamo miyalayo zinali zagolide. Anakupangira zonsezi pa tsiku limene unalengedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa