Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.
Eksodo 39:18 - Buku Lopatulika Ndi nsonga zake ziwiri zina za maunyolo awiri opotawo anazimanga pa zoikamo ziwiri, nazimanga pa zapamapewa za efodi, m'tsogolo mwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi nsonga zake ziwiri zina za maunyolo awiri opotawo anazimanga pa zoikamo ziwiri, nazimanga pa zapamapewa za efodi, m'tsogolo mwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndi kulumikiza nsonga ziŵiri zina za zingwezo m'zoikamo zake ziŵiri zija. Motero adazilumikiza patsogolo pa tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo mbali ina ya timaunyoloto anamangirira pa zoyikapo zake ziwiri zija, ndi kulumikiza pa tinsalu takutsogolo kwa mapewa a efodi. |
Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.
ndi maunyolo awiri a golide woona; uwapote ngati zingwe, ntchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo.
Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolide, naziika pansonga ziwiri za chapachifuwa, m'mphepete mwake m'katimo, pa mbali ya kuefodi.
Masaya ako akongola ndi nkhata zatsitsi, ndi khosi lako ndi zinganga za mkanda wonyezimira.