Ndipo uliyengere mphete zinai zagolide, ndi kuziika kumiyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake ina, ndi mphete ziwiri pa ina.
Eksodo 39:16 - Buku Lopatulika Anapanganso zoikamo ziwiri zagolide, ndi mphete ziwiri zagolide; naika mphete ziwirizo pansonga ziwiri za chapachifuwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anapanganso zoikamo ziwiri zagolide, ndi mphete ziwiri zagolide; naika mphete ziwirizo pa nsonga ziwiri za chapachifuwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adapanganso zoikamo zake ziŵiri zagolide zonga maluŵa, ndiponso mphete ziŵiri, ndipo adalumikiza mphete ziŵirizo ku nsonga zake zapamwamba za chovala chapachifuwacho. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anapanganso zoyikamo zake zagolide ndi mphete ziwiri zagolide, ndipo anamangirira mphetezo pa ngodya ziwiri za chovala chapachifuwa. |
Ndipo uliyengere mphete zinai zagolide, ndi kuziika kumiyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake ina, ndi mphete ziwiri pa ina.
Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.