Ndipo ulipangire sefa, malukidwe ake ndi amkuwa; nupange pa malukidwewo ngodya zake zinai mphete zinai zamkuwa.
Eksodo 38:4 - Buku Lopatulika Ndipo anapangira guwa la nsembelo sefa, malukidwe ake nja mkuwa, pansi pa khoma lamkati lake wakulekeza pakati pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapangira guwa la nsembelo sefa, malukidwe ake nja mkuwa, pansi pa khoma lamkati lake wakulekeza pakati pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adapanga chitsulo cha sefa, cha guwa lansembelo, cholukidwa ndi mkuŵa wokhawokha, ndipo adachiika kunsi kwake kwa chibumi cha guwa, kuti chifike pakatimpakati pa guwalo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anapanga sefa yachitsulo chamkuwa ya guwa lansembelo kuti ikhale mmunsi mwa khoma la guwa lansembelo, kuchokera pansi mpaka pakati pa khoma la guwalo. |
Ndipo ulipangire sefa, malukidwe ake ndi amkuwa; nupange pa malukidwewo ngodya zake zinai mphete zinai zamkuwa.
Nuwaike pansi pa khoma lamkati la guwa la nsembelo posungulira, kuti malukidwe alekeze pakati pa guwa la nsembelo.
Anapanganso zipangizo zonse za guwalo, zotayira, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, ndi mitungo, ndi zopalira moto; zipangizo zake zonse anazipanga zamkuwa.