Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 38:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Anapanga sefa yachitsulo chamkuwa ya guwa lansembelo kuti ikhale mmunsi mwa khoma la guwa lansembelo, kuchokera pansi mpaka pakati pa khoma la guwalo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo anapangira guwa la nsembelo sefa, malukidwe ake nja mkuwa, pansi pa khoma lamkati lake wakulekeza pakati pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anapangira guwa la nsembelo sefa, malukidwe ake nja mkuwa, pansi pa khoma lamkati lake wakulekeza pakati pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsono adapanga chitsulo cha sefa, cha guwa lansembelo, cholukidwa ndi mkuŵa wokhawokha, ndipo adachiika kunsi kwake kwa chibumi cha guwa, kuti chifike pakatimpakati pa guwalo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 38:4
4 Mawu Ofanana  

Upange sefa yachitsulo chamkuwa ndipo mʼngodya zake zinayizo upangiremo mphete zamkuwa.


Uyike sefayo mmunsi mwa khoma la guwa lansembelo, ndipo ilekezere pakati pa guwa lansembelo.


Anapanganso ziwiya zamkuwa izi zogwirira ntchito pa guwalo: miphika, mafosholo, mabeseni owazira magazi, ngowe zokowera nyama ndi zosonkhezera moto.


Anapanga mphete zamkuwa zinayi ndipo anazilumikiza ku ngodya zinayi za sefa ija kuti zigwire nsichi zonyamulira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa