Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 38:3 - Buku Lopatulika

3 Anapanganso zipangizo zonse za guwalo, zotayira, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, ndi mitungo, ndi zopalira moto; zipangizo zake zonse anazipanga zamkuwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Anapanganso zipangizo zonse za guwalo, zotayira, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, ndi mitungo, ndi zopalira moto; zipangizo zake zonse anazipanga zamkuwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Adapanganso zipangizo zonse za guwalo, mbale zolandirira phulusa, mafosholo, mabeseni, ngoŵe zokoŵera zinthu, ndiponso ziwaya zosonkhapo moto. Zonsezo zidapangidwa ndi mkuŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Anapanganso ziwiya zamkuwa izi zogwirira ntchito pa guwalo: miphika, mafosholo, mabeseni owazira magazi, ngowe zokowera nyama ndi zosonkhezera moto.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 38:3
6 Mawu Ofanana  

Miphika yomwe, ndi zoolera, ndi mitungo, ndi zipangizo zake zonse, Huramuabi anazipangira mfumu Solomoni, kuzipangira nyumba ya Yehova, za mkuwa wonyezimira.


Anayenganso thawale losungunula la mikono khumi kukamwa, lozunguniza, ndi msinkhu wake mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizunguniza.


Ndipo uzipanga zotayira zake zakulandira mapulusa ake, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake, ndi mitungo yake, ndi zopalira moto zake; zipangizo zake zonse uzipanga zamkuwa.


Ndipo anapanga nyanga zake pangodya zake zinai; nyanga zake zinakhala zotuluka m'mwemo; ndipo analikuta ndi mkuwa.


Ndipo anapangira guwa la nsembelo sefa, malukidwe ake nja mkuwa, pansi pa khoma lamkati lake wakulekeza pakati pake.


Ndipo machitidwe a ansembe akuchitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu aliyense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama ili chiwirire, ndi chovuulira cha ngowe cha mano atatu m'dzanja lake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa