Ndipo analota, taonani, makwerero anaima pansi, pamwamba pake ndipo padafikira kumwamba: ndipo, taonani, amithenga a Mulungu analinkukwera, analinkutsika pamenepo.
Eksodo 37:9 - Buku Lopatulika Ndipo akerubi anafunyulira mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zopenyana; zinapenya kuchotetezerapo nkhope zao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akerubi anafunyulira mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zopenyana; zinapenya kuchotetezerapo nkhope zao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mapiko a akerubiwo adaŵatambalitsa pamwamba, kuphimba chivundikiro chija. Adakhala choyang'anana, ndipo aliyense anali kuyang'anananso ndi chivundikirocho. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mapiko a Akerubiwo anatambasukira pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo kuti achiphimbe. Akerubiwo anakhala choyangʼanana, aliyense kuyangʼana chivundikirocho. |
Ndipo analota, taonani, makwerero anaima pansi, pamwamba pake ndipo padafikira kumwamba: ndipo, taonani, amithenga a Mulungu analinkukwera, analinkutsika pamenepo.
Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.
Ndipo anaika akerubiwo m'chipinda cha m'katimo, ndi mapiko a akerubiwo anatambasuka kotero kuti phiko lake la kerubi mmodzi linajima ku khoma limodzi, ndipo phiko la kerubi wina linajima khoma lina, ndi mapiko ao anagundana pakati pa nyumba.
Ndipo akerubi afunyululire mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zipenyane; nkhope za akerubi zipenye kuchotetezerapo.
Ndipo anapanga gome la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri, ndi kupingasa kwake mkono umodzi, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu;
kerubi mmodzi pa mbali yake imodzi, ndi kerubi wina pa mbali yake ina; anapanga akerubi ochokera m'chotetezerapo, pa mathungo ake awiri.
Pamwamba pa Iye panaima aserafi; yense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi; awiri anaphimba nao nkhope yake, awiri naphimba nao mapazi ake, awiri nauluka nao.
Ndipo ananena naye, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mudzaona thambo lotseguka, ndi angelo a Mulungu akwera natsikira pa Mwana wa Munthu.
Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kunka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu.
kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu,
Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,
Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.
Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?
Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.