Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 25:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo akerubi afunyululire mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zipenyane; nkhope za akerubi zipenye kuchotetezerapo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo akerubi afunyululire mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zipenyane; nkhope za akerubi zipenye kuchotetezerapo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Mapiko a akerubiwo adzatambasukire pamwamba pa chivundikirocho, kuti adzachiphimbe. Akerubi adzakhale choyang'anana, aliyense kumayang'ana chivundikirocho.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Mapiko a Akerubiwo adzatambasukire pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo kuti achiphimbe. Akerubiwo adzakhale choyangʼanana, aliyense kuyangʼana chivundikirocho.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 25:20
22 Mawu Ofanana  

Ndipo analota, taonani, makwerero anaima pansi, pamwamba pake ndipo padafikira kumwamba: ndipo, taonani, amithenga a Mulungu analinkukwera, analinkutsika pamenepo.


Ndipo m'chipinda chamkatimo anasema mitengo ya azitona akerubi awiri, yense wa msinkhu wake mikono khumi.


Ndipo anaika akerubiwo m'chipinda cha m'katimo, ndi mapiko a akerubiwo anatambasuka kotero kuti phiko lake la kerubi mmodzi linajima ku khoma limodzi, ndipo phiko la kerubi wina linajima khoma lina, ndi mapiko ao anagundana pakati pa nyumba.


Popeza akerubiwo anatambasula mapiko ao awiri pamwamba pa likasa, ndipo akerubiwo anaphimba pamwamba pa likasa ndi mphiko zake.


ndi cha guwa la nsembe lofukizapo la golide woyengetsa woyesedwa kulemera kwake, ndi chifaniziro cha galeta wa akerubi agolide akufunyulula mapiko ao ndi kuphimba likasa la chipangano la Yehova.


Ndipo m'malo opatulika kwambiri anapanga akerubi awiri, anachita osema, nawakuta ndi golide.


Uzipanganso akerubi awiri agolide; uwasule mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo.


Nupange kerubi mmodzi ku thungo lino, ndi kerubi wina ku thungo lina; upange akerubi ochokera kuchotetezerapo, pa mathungo ake awiri.


Kuli konse mzimu ukuti umuke, zinamuka komwe mzimu ukuti umuke; ndi njingazi zinanyamuka pambali pa izi; pakuti mzimu wa zamoyozo unali m'njingazo.


Unali kerubi wodzozedwa wakuphimba, ndipo ndinakuika unali paphiri lopatulika la Mulungu, anayendayenda pakati pa miyala yamoto.


Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.


Ndipo ananena naye, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mudzaona thambo lotseguka, ndi angelo a Mulungu akwera natsikira pa Mwana wa Munthu.


koma mkazi chifukwa cha mwamuna; chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pake, chifukwa cha angelo.


Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife choonetsedwa kudziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.


kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu,


ndipo muli odzazidwa mwa Iye, ndiye mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro;


Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?


ndi pamwamba pake akerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo; za izi sitingathe kunena tsopano paderapadera.


Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.


amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa