Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.
Eksodo 34:2 - Buku Lopatulika Nukonzekeretu m'mawa, nukwere m'mawa m'phiri la Sinai, nuimepo pamaso panga pamwamba paphiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nukonzekeretu m'mawa, nukwere m'mawa m'phiri la Sinai, nuimepo pamaso panga pamwamba pa phiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ukonzeke m'mamaŵa, ndipo nthaŵi yam'maŵa, ukwere phiri la Sinai kuti udzakumane nane pamwamba pa phiripo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ukonzeke mmamawa, ndipo ubwere ku Phiri la Sinai. Udzaonekera pamaso panga pamwamba pa phiri. |
Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.
Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.
Ndipo Yehova anatsikira paphiri la Sinai, pamutu pake paphiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu paphiri; ndi Mose anakwerapo.
Ndipo Yehova anati kwa iye, Muka, tsika; nukwere iwe ndi Aroni pamodzi ndi iwe; koma ansembe ndi anthu asapyole kukwera kwa Yehova, angawapasule.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo ndi malamulo ndawalembera kuti uwalangize.
Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova masiku makumi anai usana ndi usiku ndinagwa pansiwa; popeza Yehova adati kuti adzakuonongani.