Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 34:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ukonzeke mmamawa, ndipo ubwere ku Phiri la Sinai. Udzaonekera pamaso panga pamwamba pa phiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Nukonzekeretu m'mawa, nukwere m'mawa m'phiri la Sinai, nuimepo pamaso panga pamwamba paphiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nukonzekeretu m'mawa, nukwere m'mawa m'phiri la Sinai, nuimepo pamaso panga pamwamba pa phiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ukonzeke m'mamaŵa, ndipo nthaŵi yam'maŵa, ukwere phiri la Sinai kuti udzakumane nane pamwamba pa phiripo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 34:2
6 Mawu Ofanana  

ndipo akhale atakonzeka pofika tsiku lachitatu, chifukwa tsiku limenelo Yehova adzatsika pa phiri la Sinai anthu onse akuona.


Phiri la Sinai linakutidwa ndi utsi, chifukwa Yehova anatsika ndi moto pa phiripo. Utsi unakwera ngati wochokera mʼngʼanjo yamoto ndipo phiri lonse linagwedezeka kwambiri.


Yehova anatsika nafika pamwamba pa phiri la Sinai, ndipo anayitana Mose kuti apite pa phiripo. Choncho Mose anakwera,


Yehova anayankha, “Tsika ukamutenge Aaroni. Koma ansembe ndi anthu asayesere kubzola malire kuti abwere kwa Yehova chifukwa Iye adzawalanga.”


Yehova anati kwa Mose, “Bwera kwa ine ku phiri kuno, ndipo udikire konkuno. Ndidzakupatsa miyala imene ndalembapo malemba kuti ndiwaphunzitse.”


Ine ndinagwa chafufumimba pamaso pa Yehova kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku chifukwa Yehova ananena kuti akuwonongani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa