Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 19:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo Yehova anati kwa iye, Muka, tsika; nukwere iwe ndi Aroni pamodzi ndi iwe; koma ansembe ndi anthu asapyole kukwera kwa Yehova, angawapasule.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo Yehova anati kwa iye, Muka, tsika; nukwere iwe ndi Aroni pamodzi ndi iwe; koma ansembe ndi anthu asapyole kukwera kwa Yehova, angawapasule.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Tsono Chauta adauza Moseyo kuti, “Tsika pansi, ndipo ukamtenge Aroni, ubwere naye kuno. Koma ansembe pamodzi ndi anthu asabzole malirewo kubwera kwa Ine kuno, kuti ndingadzaŵalange.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Yehova anayankha, “Tsika ukamutenge Aaroni. Koma ansembe ndi anthu asayesere kubzola malire kuti abwere kwa Yehova chifukwa Iye adzawalanga.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 19:24
20 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene anafika ku dwale la Kidoni, Uza anatambasula dzanja lake kulichirikiza likasa, pakuti ng'ombe zikadapulumuka.


Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzichenjera musakwere m'phiri, musakhudza malire ake; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;


Pamenepo Mose anawatsikira anthu, nanena nao.


Ndipo Iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri; ndipo mugwadire pakudza kutali;


Ndipo Mose ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri anakwerako;


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete.


Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokakamizidwa, ndipo okakamirawo aukwatula ndi mphamvu.


Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza.


Chilamulo ndi aneneri analipo kufikira pa Yohane; kuyambira pamenepo ulalikidwa Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo munthu aliyense akangamira kulowamo.


Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.


pakuti chilamulo chichitira mkwiyo; koma pamene palibe lamulo, pamenepo palibe kulakwa.


Nanga chilamulo tsono? Chinaonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbeu imene adailonjezera; ndipo chinakonzeka ndi angelo m'dzanja la nkhoswe.


Komatu lembo linatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo.


Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.


Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa