ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Eksodo 34:16 - Buku Lopatulika ndipo ungatengereko ana ako aamuna ana ao akazi; nangachite chigololo ana ao aakazi potsata milungu yao, ndi kuchititsa ana anu amuna chigololo potsata milungu yao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo ungatengereko ana ako amuna ana ao akazi; nangachite chigololo ana ao akazi potsata milungu yao, ndi kuchititsa ana anu amuna chigololo potsata milungu yao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwina ana anu aamuna angathenso kumadzakwatira ana ao aakazi. Tsono akazi ameneŵa akamadziipitsa potumikira milungu yao, adzakopa ana anu aamuna kuti azidzatumikiranso milungu yaoyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo inu mukasankha ena mwa ana awo aakazi kukhala akazi a ana anu, akaziwo akakachita zadama ndi milungu yawo, akatsogolera ana anu aamuna kuchita chimodzimodzi. |
ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao.
Ndipo mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo, pamodzi ndi mwana wamkazi wa Farao, akazi a ku Mowabu, ndi a ku Amoni, ndi a ku Edomu, ndi a ku Sidoni, ndi Ahiti;
Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, amene Yezebele mkazi wake anamfulumiza.
Anamanganso misanje m'mapiri a Yuda, nachititsa okhala mu Yerusalemu chigololo, nakankhirako Ayuda.
Chifukwa chake tsono, musamapereka ana anu akazi kwa ana ao aamuna, kapena kutengera ana anu aamuna ana ao akazi, kapena kufuna mtendere wao ndi kukoma kwao nthawi yonse, kuti mukhale olimba, ndi kudya zokoma za m'dziko, ndi kulisiyira ana anu cholowa cha kunthawi yonse.
Pakuti anadzitengera okha ndi ana aamuna ao ana aakazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene.
ndi kuti sitidzapereka ana athu aakazi kwa mitundu ya anthu a m'dziko, kapena kutengera ana athu aamuna ana ao aakazi;
ndipo mitundu ya anthu a m'dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, tsiku la Sabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao pa tsiku la Sabata, kapena tsiku lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka chaka chachisanu ndi chiwiri ndi mangawa ali onse.
Ndipo ndinatsutsana nao, ndi kuwatemberera, ndi kukantha ena a iwo, ndi kumwetula tsitsi lao, ndi kuwalumbiritsa pa Mulungu ndi kuti, Musapereke ana anu aakazi kwa ana ao aamuna, kapena kutengera ana anu aamuna, kapena a inu nokha, ana ao aakazi.
Chiyambi cha kunena kwa Yehova mwa Hoseya. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wachigololo ndi ana achigololo; pakuti dziko latsata chigololo chokhachokha kuleka kutsata Yehova.
Koma, mukadzabwerera m'mbuyo pang'ono pokha ndi kuumirira otsala a mitundu awa, ndiwo akutsala pakati pa inu, ndi kukwatitsana nao, ndi kulowana nao, naonso kulowana nanu;
dziwani ndithu kuti Yehova Mulungu wanu sadzalandanso dziko la amitundu awa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala kwa inu deka ndi msampha ndi mkwapulo m'nthiti mwanu, ndi minga m'maso mwanu, mpaka mudzatayika m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.
Koma atate wake ndi amai wake ananena naye, Kodi palibe mkazi mwa ana aakazi a abale ako, kapena mwa anthu a mtundu wanga onse, kuti wamuka kutenga mkazi wa Afilisti osadulidwawo? Nati Samisoni kwa atate wake, Nditengereni iye, pakuti andikonda pamaso panga.
Ndipo ana a Israele anakhala pakati pa Akanani, Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi;
nakwatira ana aakazi a iwowa, napereka ana ao akazi kwa ana aamuna a iwowa natumikira milungu yao.
Ndipo Gideoni anawapanga fano, naliika m'mzinda mwake, ndiwo Ofura; ndi Israele yense analitsata kuligwadira pomwepo; ndipo linakhala kwa Gideoni ndi nyumba yake ngati msampha.