Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 13:23 - Buku Lopatulika

23 Masiku aja ndinaonanso Ayudawo anadzitengera akazi a Asidodi, Aamoni, ndi Amowabu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Masiku aja ndinaonanso Ayudawo anadzitengera akazi a Asidodi, Aamoni, ndi Amowabu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Nthaŵi imeneyo ndidaona Ayuda amene adaakwatira akazi a ku Asidodi, a ku Amoni ndiponso a ku Mowabu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Masiku amenewo ndinaonanso anthu a ku Yuda amene anakwatira akazi ochokera ku Asidodi, Amoni ndi Mowabu.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 13:23
16 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo, pamodzi ndi mwana wamkazi wa Farao, akazi a ku Mowabu, ndi a ku Amoni, ndi a ku Edomu, ndi a ku Sidoni, ndi Ahiti;


Pamenepo Ezara wansembe ananyamuka, nanena nao, Mwalakwa, mwadzitengera akazi achilendo, kuonjezera kupalamula kwa Israele.


Awa onse adatenga akazi achilendo, ndi ena a iwowa anali ndi akazi amene adawabalira ana.


ndi kuti sitidzapereka ana athu aakazi kwa mitundu ya anthu a m'dziko, kapena kutengera ana athu aamuna ana ao aakazi;


ndipo mitundu ya anthu a m'dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, tsiku la Sabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao pa tsiku la Sabata, kapena tsiku lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka chaka chachisanu ndi chiwiri ndi mangawa ali onse.


Tsiku lomwelo anawerenga m'buku la Mose m'makutu a anthu, napeza m'menemo kuti Aamoni ndi Amowabu asalowe mu msonkhano wa Mulungu kunthawi yonse;


ndi ana ao analankhula mwina Chiasidodi, osadziwitsa kulankhula Chiyuda, koma monga umo amalankhula mtundu wao uliwonse.


Ndipo kodi tidzamvera inu, kuchita choipa ichi chachikulu chonse, kulakwira Mulungu wathu ndi kudzitengera akazi achilendo?


Koma kunali, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Aarabu, ndi Aamoni, ndi Aasidodi, kuti makonzedwe a malinga a Yerusalemu anakula, ndi kuti mopasuka mwake munayamba kutsekeka, chidawaipira kwambiri;


Dzisungire chimene Ine ndikuuza lero lino: taona, ndiingitsa pamaso pako Aamori ndi Akanani, ndi Ahiti ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.


Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?


Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu, ndipo atakataya amitundu ambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikulu ndi yamphamvu yoposa inu;


Nadzitengera iwo akazi a ku Mowabu; wina dzina lake ndiye Oripa, mnzake dzina lake ndiye Rute; ndipo anagonera komweko ngati zaka khumi.


Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa