Nehemiya 13:22 - Buku Lopatulika22 Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Kenaka ndidaŵalamula Alevi kuti adziyeretse ndipo abwere kudzalonda pa zipata, kuti tsiku la sabata lisungike ngati lopatulika. Inu Mulungu wanga, mukumbukire zimenezinso pondikomera mtima, ndipo mundisunge potsata chikondi chanu chachikulu chosasinthika. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Ndipo ndinalamulira Alevi kuti adziyeretse okha ndi kubwera kudzalonda pa zipata ndi cholinga choti tsiku la Sabata likhale tsiku loyera. Inu Mulungu wanga, kumbukireninso ine pa zimenezi ndipo mundisunge malingana ndi chikondi chanu chachikulu chosasinthika. Onani mutuwo |
Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo lachiwiri, ndi olindira pakhomo, atulutse mu Kachisi wa Yehova zipangizo adazipangira Baala, ndi chifanizo adazipangira Baala, ndi chifanizo chija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lake kunka nalo ku Betele.