Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 10:30 - Buku Lopatulika

30 ndi kuti sitidzapereka ana athu aakazi kwa mitundu ya anthu a m'dziko, kapena kutengera ana athu aamuna ana ao aakazi;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 ndi kuti sitidzapereka ana athu akazi kwa mitundu ya anthu a m'dziko, kapena kutengera ana athu amuna ana ao akazi;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Sitidzapereka ana athu aakazi kuti akakwatiwe ndi anthu a mitundu ina ya m'dzikomo, sitidzalolanso ana athu aamuna kuti akakwatire ana ao aakazi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 “Ife tikulonjeza kuti sitidzapereka ana athu aakazi kuti akwatiwe ndi amuna a mayiko ena kapena kutenga ana awo aakazi kuti akwatiwe ndi ana athu aamuna.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 10:30
15 Mawu Ofanana  

Ndipo asanabadwe iye panalibe mfumu wolingana naye, imene inatembenukira kwa Yehova ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi mphamvu yake yonse, monga mwa chilamulo chonse cha Mose; atafa iyeyu sanaukenso wina wolingana naye.


Niima mfumu pachiunda, ndi kuchita pangano pamaso pa Yehova, kutsata Yehova ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukhazikitsa mau a chipangano cholembedwa m'buku ili; ndipo anthu onse anaimiririra panganoli.


Ndipo mfumu inaimirira pokhala pake, ndi kuchita pangano pamaso pa Yehova, kuti adzayenda chotsata Yehova, ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, kuchita mau a chipangano olembedwa m'bukumu.


Okhomera chizindikiro tsono ndiwo Nehemiya, Tirisata mwana wa Hakaliya, ndi Zedekiya,


Masiku aja ndinaonanso Ayudawo anadzitengera akazi a Asidodi, Aamoni, ndi Amowabu,


Ndipo ndinatsutsana nao, ndi kuwatemberera, ndi kukantha ena a iwo, ndi kumwetula tsitsi lao, ndi kuwalumbiritsa pa Mulungu ndi kuti, Musapereke ana anu aakazi kwa ana ao aamuna, kapena kutengera ana anu aamuna, kapena a inu nokha, ana ao aakazi.


Momwemo ndinawayeretsa kuwachotsera achilendo onse, ndi kuikira udikiro ansembe ndi Alevi, yense kuntchito yake;


Pamenepo anati, Tidzawabwezera osawalipitsa kanthu, tidzachita monga momwe mwanena. Pamenepo ndinaitana ansembe, ndi kuwalumbiritsa, kuti adzachita monga mwa mau awa.


Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama.


ndipo ungatengereko ana ako aamuna ana ao akazi; nangachite chigololo ana ao aakazi potsata milungu yao, ndi kuchititsa ana anu amuna chigololo potsata milungu yao.


makanda anu, akazi anu, ndi mlendo wanu wakukhala pakati pa zigono zanu, kuyambira wotema nkhuni kufikira wotunga madzi;


Ndipo musakwatitsane nao; musampatse mwana wake wamwamuna mwana wanu wamkazi, kapena kutenga mwana wake wamkazi akhale wa mwana wanu wamwamuna.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa