Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 11:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo, pamodzi ndi mwana wamkazi wa Farao, akazi a ku Mowabu, ndi a ku Amoni, ndi a ku Edomu, ndi a ku Sidoni, ndi Ahiti;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo, pamodzi ndi mwana wamkazi wa Farao, akazi a ku Mowabu, ndi a ku Amoni, ndi a ku Edomu, ndi a ku Sidoni, ndi Ahiti;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mfumu Solomoni ankakonda akazi ambiri achilendo. Kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao, adakwatiranso akazi a mitundu iyi: Amowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni ndi Ahiti.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Komatu Mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo ndipo kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao, analinso ndi akazi a mitundu iyi: Amowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni, ndi Ahiti.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 11:1
20 Mawu Ofanana  

Ndipo momwemo anachitiranso akazi ake onse achilendo, amene amafukizira naphera nsembe milungu yao.


Ndipo Rehobowamu mwana wa Solomoni anali mfumu ya dziko la Yuda. Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri mu Yerusalemu, m'mzinda m'mene Yehova adausankha m'mafuko onse a Israele kukhazikamo dzina lake. Ndipo dzina la amake linali Naama Mwamoni.


Nagona Rehobowamu ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m'mzinda wa Davide. Ndipo dzina la amake linali Naama Mwamoni, nalowa ufumu m'malo mwake Abiya mwana wake.


Ndipo kunali monga ngati kunamchepera kuyenda m'machimo a Yerobowamu mwana wa Nebati, iye anakwatira Yezebele mwana wamkazi wa Etibaala mfumu ya Asidoni, natumikira Baala, namgwadira.


Ndipo Solomoni anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aejipito, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye kumzinda wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu.


Awa onse adatenga akazi achilendo, ndi ena a iwowa anali ndi akazi amene adawabalira ana.


Zitatha izi tsono anandiyandikira akalonga, ndi kuti, Anthu a Israele, ndi nsembe, ndi Alevi, sanadzilekanitse ndi anthu a maikowa, kunena za zonyansa zao za Akanani, Ahiti, Aperizi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aejipito, ndi Aamori.


Pakuti anadzitengera okha ndi ana aamuna ao ana aakazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene.


ndipo ungatengereko ana ako aamuna ana ao akazi; nangachite chigololo ana ao aakazi potsata milungu yao, ndi kuchititsa ana anu amuna chigololo potsata milungu yao.


Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere, kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake;


M'kamwa mwa mkazi wachiwerewere muli dzenje lakuya; yemwe Yehova amkwiyira adzagwamo.


Maso ako adzaona zachilendo, mtima wako udzalankhula zokhota.


Musapereke mphamvu yako kwa akazi, ngakhale kuyenda m'njira yoononga mafumu.


Zikutchinjiriza kwa mkazi woipa, ndi kulilime losyasyalika la mkazi wachiwerewere.


Kuti zikutchinjirizire kwa mkazi wachiwerewere, kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ake.


Usamtenga mkazi kumuonjezera kwa mbale wake, kumvula, kumvula pamodzi ndi mnzake, akali ndi moyo mnzakeyo.


Ndipo asadzichulukitsire akazi, kuti ungapatuke mtima wake; kapena asadzichulukitsire kwambiri siliva ndi golide.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa