Eksodo 34:1 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa Mose, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja; ndipo ndidzalembera pa magomewo mau omwewo anali pa magome oyambawo, amene unawaswa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja; ndipo ndidzalembera pa magomewo mau omwewo anali pa magome oyambawo, amene unawaswa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauzanso Mose kuti, “Sema ina miyala ngati iŵiri yakale ija, kuti ndilembepo mau omwe anali pa miyala yoyamba udaphwanya ija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anati kwa Mose, “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo Ine ndidzalembapo mawu amene anali pa miyala yoyamba ija, imene unayiphwanya. |
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo ndi malamulo ndawalembera kuti uwalangize.
Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, paphiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.
Ndipo magomewo ndiwo ntchito ya Mulungu, kulembaku ndiko kulemba kwa Mulungu, kozokoteka pa magomewo.
Ndipo kunali, pamene anayandikiza chigono, anaona mwanawang'ombeyo ndi kuvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwake, nawaswa m'tsinde mwa phiri.
Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadye mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mau a panganolo, mau khumiwo.
Ndipo anasema magome awiri a miyala, onga oyamba aja; ndipo Mose anauka mamawa nakwera m'phiri la Sinai, monga Yehova adamuuza, nagwira m'dzanja mwake magome awiri amiyala.
Ndipo Yeremiya anatenga mpukutu wina, naupereka kwa Baruki mlembi, mwana wa Neriya; amene analemba m'menemo ponena Yeremiya mau onse a m'buku lija Yehoyakimu mfumu ya Yuda analitentha m'moto; ndipo anaonjezapo mau ambiri oterewa.
Pamenepo anakufotokozerani chipangano chake, chimene anakulamulirani kuchichita, ndiwo Mau Khumi; nawalemba pa magome awiri amiyala.