Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?
Eksodo 31:3 - Buku Lopatulika ndipo ndamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, ndi m'ntchito zilizonse, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo ndamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, ndi m'ntchito zilizonse, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyeyu ndampatsa mzimu wanga, kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru, ndipo akudziŵa bwino ntchito zonse zaluso monga izi: Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ndamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi: |
Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?
Iyeyo anali mwana wake wa mkazi wamasiye wa fuko la Nafutali, atate wake anali munthu wa ku Tiro, mfundi wamkuwa; ndipo iye anadzala ndi nzeru ndi luntha ndi luso kugwira ntchito zonse za mkuwa. Ndipo anadza kwa mfumu Solomoni namgwirira ntchito zake zonse.
Ndipo tsono munditumizire munthu waluso lakuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi thonje lofiirira, ndi lofiira, ndi lamadzi, wakudziwa kuzokota zozokota zilizonse, akhale ndi amuna aluso okhala ndi ine mu Yuda ndi mu Yerusalemu, amene Davide atate wanga anawakonzeratu.
Ndipo ulankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zovala apatulidwe nazo, andichitire Ine ntchito ya nsembe.
ndipo anamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, za m'ntchito zilizonse;
Amenewo anawadzaza ndi luso lamtima, lakuchita ntchito zilizonse, ya kuzokota miyala, ndi ya mmisiri waluso, ndi ya wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ya muomba, ya iwo akuchita ntchito iliyonse, ndi ya iwo olingirira ntchito yaluso.
ndipo adzakhala mzimu wa chiweruziro kwa oweruza milandu, ndi mphamvu kwa iwo amene abweza nkhondo pachipata.