Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 35:31 - Buku Lopatulika

31 ndipo anamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, za m'ntchito zilizonse;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 ndipo anamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, za m'ntchito zilizonse;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Chauta wadzaza Bezaleleyo ndi mzimu wa Mulungu, kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru, ndiponso ndi wodziŵa ntchito zonse zaluso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 ndipo wamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi:

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 35:31
13 Mawu Ofanana  

Iyeyo anali mwana wake wa mkazi wamasiye wa fuko la Nafutali, atate wake anali munthu wa ku Tiro, mfundi wamkuwa; ndipo iye anadzala ndi nzeru ndi luntha ndi luso kugwira ntchito zonse za mkuwa. Ndipo anadza kwa mfumu Solomoni namgwirira ntchito zake zonse.


ndiye mwana wa munthu wamkazi wa ana aakazi a Dani, ndipo atate wake ndiye munthu wa ku Tiro, wodziwa kuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi mwala, ndi mitengo, ndi thonje lofiirira, ndi lamadzi, ndi bafuta la thonje losansitsa ndi lofiira, ndi kuzokota mazokotedwe ali onse, ndi kulingirira chopanga chilichonse; kuti ampatse pokhala pamodzi ndi aluso anu, ndi aluso a mbuye wanga Davide atate wanu.


Ndipo ulankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zovala apatulidwe nazo, andichitire Ine ntchito ya nsembe.


ndipo ndamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, ndi m'ntchito zilizonse,


Ndipo Mose anati kwa ana a Israele, Taonani, Yehova anaitana, ndi kumtchula dzina lake, Bezalele, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda;


kulingirira ntchito zaluso, kuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa;


Amenewo anawadzaza ndi luso lamtima, lakuchita ntchito zilizonse, ya kuzokota miyala, ndi ya mmisiri waluso, ndi ya wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ya muomba, ya iwo akuchita ntchito iliyonse, ndi ya iwo olingirira ntchito yaluso.


Pakuti Mulungu wake amlangiza bwino namphunzitsa.


amene zolemera zonse za nzeru ndi chidziwitso zibisika mwa Iye.


Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa