2 Mbiri 2:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo tsono munditumizire munthu waluso lakuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi thonje lofiirira, ndi lofiira, ndi lamadzi, wakudziwa kuzokota zozokota zilizonse, akhale ndi amuna aluso okhala ndi ine mu Yuda ndi mu Yerusalemu, amene Davide atate wanga anawakonzeratu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo tsono munditumizire munthu waluso lakuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi thonje lofiirira, ndi lofiira, ndi lamadzi, wakudziwa kuzokota zozokota zilizonse, akhale ndi amuna aluso okhala ndi ine m'Yuda ndi m'Yerusalemu, amene Davide atate wanga anawakonzeratu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Tsono tumizireni munthu waluso pa ntchito za golide, siliva, mkuŵa, chitsulo, nsalu yofiirira, yofiira ndi yobiriŵira, ndiponso wodziŵa kuzokota. Akhale pamodzi ndi anthu aluso amene ali ndi ine ku Yuda ndi ku Yerusalemu amene Davide bambo wanga adandipatsa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 “Tsono tumizireni munthu waluso pa ntchito zagolide ndi siliva, mkuwa ndi chitsulo, nsalu yapepo ndi yofiira ndi yobiriwira ndiponso waluso losema, kuti adzagwire ntchito mu Yuda ndi Yerusalemu pamodzi ndi anthu aluso amene abambo anga Davide anandipatsa. Onani mutuwo |