Eksodo 30:5 - Buku Lopatulika Ndipo upange mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo upange mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mphiko zimenezi ikhale ya mtengo wa kasiya, ndipo uikute ndi golide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Upange mizati yamtengo wa mkesha ndipo uyikute ndi golide. |
ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;
Ndipo ulipangire mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake; uziike pa nthiti zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo.
Nuliike chakuno cha nsalu yotchinga ili ku likasa la mboni, patsogolo pa chotetezerapo chili pamwamba pa mboni, pomwe ndidzakomana ndi iwe.