Eksodo 30:19 - Buku Lopatulika Ndipo Aroni ndi ana ake aamuna azisambiramo manja ao ndi mapazi ao; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aroni ndi ana ake amuna azisambiramo manja ao ndi mapazi ao; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aroni ndi ana ake azisamba m'manja ndi kutsuka mapazi ao ndi madzi amenewo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aaroni ndi ana ake azisamba mʼmanja ndi kutsuka mapazi awo ndi madzi amenewo. |
Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake aamuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa m'madzi.
pakulowa iwo m'chihema chokomanako asambe ndi madzi, kuti angafe; kapena poyandikiza guwa la nsembe kutumikirako, kufukiza nsembe yamoto ya Yehova;
Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babiloni; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.
zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,
tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;
Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.