Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 30:20 - Buku Lopatulika

20 pakulowa iwo m'chihema chokomanako asambe ndi madzi, kuti angafe; kapena poyandikiza guwa la nsembe kutumikirako, kufukiza nsembe yamoto ya Yehova;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 pakulowa iwo m'chihema chokomanako asambe ndi madzi, kuti angafe; kapena poyandikiza guwa la nsembe kutumikirako, kufukiza nsembe yamoto ya Yehova;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Akamaloŵa m'chihema chamsonkhano, kapena kuyandikira guwalo pa ntchito yao yautumiki, ndi kumapereka kwa Chauta chopereka chopsereza, sadzafa malinga akasamba ndi madzi amenewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Pamene akulowa mu tenti ya msonkhano, iwo asambe madziwa kuti asafe. Ndiponso pamene akupita kukatumikira ku guwa lansembe ndi kupereka nsembe yopsereza kwa Yehova,

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 30:20
14 Mawu Ofanana  

Ndi mkwiyo wa Yehova unayakira Uza, namkantha, chifukwa anatambasulira likasa dzanja lake, nafa komweko pamaso pa Mulungu.


Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.


Masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa; lingakhale tsiku loyamba muzichotsa chotupitsa m'nyumba zanu; pakuti aliyense wakudya mkate wa chotupitsa kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzachotsedwa kwa Israele.


Ndipo Aroni ndi ana ake aamuna azisambiramo manja ao ndi mapazi ao;


asambe manja ao ndi mapazi ao, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha, kwa iye ndi kwa mbeu zake, mwa mibadwo yao.


Ndipo Mose ndi Aroni ndi ana ake aamuna anasamba manja ao ndi mapazi ao m'menemo;


Avale malaya a m'kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zovala za kumiyendo pathupi pake, nadzimangire m'chuuno ndi mpango wabafuta, navale nduwira yabafuta; izi ndi zovala zopatulika; potero asambe thupi lake ndi madzi, ndi kuvala izi.


Ndipo Mose anabwera nao Aroni ndi ana ake, nawasambitsa ndi madzi.


Ndipo anagwa pansi pomwepo pa mapazi ake, namwalira; ndipo analowa anyamatawo, nampeza iye wafa, ndipo anamnyamula kutuluka naye, namuika kwa mwamuna wake.


Koma Ananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha aakulu anagwera onse akumvawo.


Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betesemesi, chifukwa anasuzumira m'likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, chifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe aakulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa