ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri.
Eksodo 3:21 - Buku Lopatulika Ndipo ndidzapatsa anthu awa ufulu pamaso pa anthu a Ejipito; ndipo kudzakhala, pamene mutuluka simudzatuluka opanda kanthu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndidzapatsa anthu awa ufulu pamaso pa anthu a Ejipito; ndipo kudzakhala, pamene mutuluka simudzatuluka opanda kanthu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aejipito ndidzaŵafeŵetsa mtima pa anthu anga, kotero kuti pamene muzidzachoka, simudzapita chimanjamanja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ndipo ine ndidzafewetsa mtima wa Aigupto pa anthu anga, kotero kuti mukadzatuluka simudzapita wopanda kanthu. |
ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri.
Koma Yehova anali ndi Yosefe namchitira iye zokoma, nampatsa ufulu pamaso pa woyang'anira kaidi.
ndi kukhululukira anthu anu adachimwira Inu ndi mphulupulu zao zonse adapalamula nazo kwa Inu; ndipo muwachititsire chifundo iwo amene anawagwira ndende, kuti awachitire chifundo;
Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.
Ndipo anawatulutsa pamodzi ndi siliva ndi golide: ndi mwa mafuko ao munalibe mmodzi wokhumudwa.
Lankhula tsopano m'makutu a anthu, kuti mwamuna yense apemphe kwa mnzake, ndi mkazi yense kwa mnzake, zokometsera zasiliva ndi zagolide.
Ndipo Yehova anawapatsa anthu chisomo pamaso pa Aejipito. Munthuyo Mose ndiyenso wamkulu ndithu m'dziko la Ejipito, pamaso pa anyamata a Farao, ndi pamaso pa anthu.
Ndipo ana a Israele anachita monga mwa mau a Mose; napempha Aejipito zokometsera zasiliva, ndi zagolide, ndi zovala.
Ndipo Yehova anapatsa anthu chisomo pamaso pa Aejipito, ndipo sanawakanize. Ndipo anawafunkhira Aejipito.
namlanditsa iye m'zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse.