Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 3:22 - Buku Lopatulika

22 koma mkazi yense adzafunse mnzake, ndi mlendo wokhala m'nyumba mwake, ampatse zokometsera zasiliva, ndi zokometsera zagolide, ndi zovala; ndipo mudzaveke nazo ana anu aamuna ndi aakazi; ndipo mudzafunkhe za Aejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 koma mkazi yense adzafunse mnzake, ndi mlendo wokhala m'nyumba mwake, ampatse zokometsera zasiliva, ndi zokometsera zagolide, ndi zovala; ndipo mudzaveke nazo ana anu aamuna ndi aakazi; ndipo mudzafunkhe za Aejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Mkazi aliyense adzapempha Mwejipito woyandikana naye ndiponso amene amakhala naye m'nyumba, kuti ampatse zinthu zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide, ndiponso zovala. Zimenezi mudzaveka ana anu aamuna ndi aakazi, motero mudzaŵalanda zonse Aejipitowo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Mkazi aliyense adzapemphe Mwigupto woyandikana naye ndiponso mkazi amene akukhala mʼnyumba yake, kuti amupatse ziwiya za siliva ndi golide ndiponso zovala zimene mudzaveka ana anu aamuna ndi aakazi. Ndipo potero mudzawalanda zonse Aiguptowo.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 3:22
9 Mawu Ofanana  

ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri.


Ndipo mnyamatayo anatulutsa zokometsera zasiliva ndi zagolide, ndi zovala, nampatsa Rebeka: ndipo anapatsa za mtengo wapatali kwa mlongo wake ndi amake.


Ndipo anawatulutsa pamodzi ndi siliva ndi golide: ndi mwa mafuko ao munalibe mmodzi wokhumudwa.


Lankhula tsopano m'makutu a anthu, kuti mwamuna yense apemphe kwa mnzake, ndi mkazi yense kwa mnzake, zokometsera zasiliva ndi zagolide.


Wabwino asiyira zidzukulu zake cholowa chabwino; koma wochimwa angosungira wolungama chuma chake.


Tsoka kwa iwe amene usakaza, chinkana sunasakazidwe; nupangira chiwembu, chinkana sanakupangire iwe chiwembu! Utatha kusakaza, iwe udzasakazidwa; ndipo utatha kupangira chiwembu, iwo adzakupangira iwe chiwembu.


osatenga nkhuni kuthengo, kapena kuzitema kunkhalango; popeza adzasonkha moto ndi zidazo; nadzafunkha iwo amene anawafunkha, ndi kulanda zao za iwo adalanda zaozo, ati Ambuye Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa