Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.
Eksodo 28:25 - Buku Lopatulika Koma nsonga zake ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma nsonga zake ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo nsonga zake zina ziŵiri za zingwezo uzimange ku zoikamo zake zija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo mbali ina ya timaunyoloto umangirire pa zoyikapo zake ziwiri zija ndi kulumikiza pa tinsalu takutsogolo kwa mapewa a efodi. |
Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.
ndi maunyolo awiri a golide woona; uwapote ngati zingwe, ntchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo.
Ndipo upange mphete ziwiri zagolide, ndi kuzimanga pansonga zake ziwiri za chapachifuwa, m'mphepete mwake, m'katimo ku mbali ya kuefodi.