Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 28:24 - Buku Lopatulika

24 Numange maunyolo awiri opota agolide ku mphete ziwirizo pansonga pake pa chapachifuwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Numange maunyolo awiri opota agolide ku mphete ziwirizo pa nsonga pake pa chapachifuwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Umange zingwe zagolide ziŵiri ku mphete ziŵirizo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Umangirire timaunyolo tiwiri tagolide tija pa mphete za pa ngodya pa chovala chapachifuwacho.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:24
5 Mawu Ofanana  

Ndipo panali maukonde olukaluka ndi zoyangayanga, zokolana za pa mitu imene inali pamwamba pa nsanamira; zisanu ndi ziwiri za pamutu wina, ndi zisanu ndi ziwiri za pamutu unzake.


M'mwemo anapanga nsanamira, ndipo panali mizere iwiri yozungulira ukonde umodzi, kukuta ndi makangaza mituyi inali pamwambapo, nachita momwemo ndi mutu winawo.


ndi maunyolo awiri a golide woona; uwapote ngati zingwe, ntchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo.


Nupangire pa chapachifuwa mphete ziwiri zagolide, ndi kuzika mphete ziwirizo pansonga zake ziwiri za chapachifuwa.


Koma nsonga zake ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa