Ndipo uziomba nsalu yotsekera pa khomo la hema, ya lakuda, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula.
Eksodo 27:14 - Buku Lopatulika Ndi nsalu zotchingira za pa mbali imodzi ya kuchipata zikhale za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi nsalu zochingira za pa mbali imodzi ya kuchipata zikhale za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa mbali ina ya chipata pakhale nsalu zochinga, kutalika kwake mamita asanu ndi aŵiri, ndi nsanamira zitatu ndi masinde atatu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mbali imodzi yachipata kukhale nsalu yotchinga yotalika mamita asanu ndi awiri, mizati itatu ndi matsinde atatu. |
Ndipo uziomba nsalu yotsekera pa khomo la hema, ya lakuda, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula.
Ndipo m'kupingasa kwake kwa bwalo pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mukhale mikono makumi asanu.
Ndi pa mbali ina pakhale nsalu zotchingira za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu.
Upangenso bwalo la chihema; pa mbali yake ya kumwera, kumwera, pakhale nsalu zotchingira za kubwalo za nsalu yabafuta wa thonje losansitsa, utali wake wa pa mbali imodzi mikono zana;
Nsalu zotchingira za pa mbali imodzi ya chipata nza mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu;