Ndipo uzipanga nyali zake, zisanu ndi ziwiri; ndipo ayatse nyali zake, ziwale pandunji pake.
Eksodo 25:6 - Buku Lopatulika mafuta akuunikira, zonunkhira za mafuta odzoza, ndi za chofukiza cha fungo lokoma; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 mafuta akuunikira, zonunkhira za mafuta odzoza, ndi za chofukiza cha fungo lokoma; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa mafuta a nyale, zonunkhira za mafuta odzozera, ndiponso lubani wa fungo lokoma. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mafuta anyale a olivi, zonunkhiritsa mafuta odzozera ndi zopangira lubani wonunkhira; |
Ndipo uzipanga nyali zake, zisanu ndi ziwiri; ndipo ayatse nyali zake, ziwale pandunji pake.
ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;
Ndipo uuze ana a Israele akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza.
Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa chihema chonse, ndi zonse zili m'mwemo, malo opatulika, ndi zipangizo zake.