Ndipo Farao anachotsa mphete yosindikizira yake padzanja lake, naiveka padzanja la Yosefe, namveka iye ndi zovalira zabafuta, naika unyolo wagolide pakhosi pake;
Eksodo 25:4 - Buku Lopatulika ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira, nsalu zokoma zathonje, nsalu zopangidwa ndi ubweya wambuzi, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa, ubweya wambuzi; |
Ndipo Farao anachotsa mphete yosindikizira yake padzanja lake, naiveka padzanja la Yosefe, namveka iye ndi zovalira zabafuta, naika unyolo wagolide pakhosi pake;
ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;
Ndipo atenge golide, ndi lamadzi ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Naombe efodi ndi golide, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya mmisiri.
Ndinakuvekanso ndi nsalu zopikapika, ndi kukuveka nsapato za chikopa cha katumbu; ndinakuzenenga nsalu yabafuta, ndi kukuphimba ndi nsalu yasilika.
Thanga lako ndi labafuta wopikapika wa ku Ejipito, likhale ngati mbendera yako; chophimba chako ndicho nsalu yamadzi ndi yofiirira zochokera ku zisumbu za Elisa.
Ndipo anampatsa iye avale bafuta wonyezimira woti mbuu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.