Eksodo 24:15 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anakwera m'phirimo, ndi mtambo unaphimba phirilo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anakwera m'phirimo, ndi mtambo unaphimba phirilo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mose adakwera phiri, ndipo phirilo lidaphimbidwa ndi mtambo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose atakwera ku phiri kuja mtambo unaphimba phirilo. |
Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.
Ndipo Yehova anatsikira paphiri la Sinai, pamutu pake paphiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu paphiri; ndi Mose anakwerapo.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akuvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.
Ndipo ulemerero wa Yehova unakhalabe paphiri la Sinai, ndi mtambo unaliphimba masiku asanu ndi limodzi; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri Iye ali m'kati mwa mtambo anaitana Mose.
Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.