Ndidzawaingitsa pang'onopang'ono pamaso pako, kufikira utachuluka, ndi kulandira dziko cholowa chako.
Eksodo 23:29 - Buku Lopatulika Sindidzawaingitsa pamaso pako chaka chimodzi; kuti dziko lingakhale bwinja, ndi zilombo zakuthengo zingakuchulukire. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sindidzawaingitsa pamaso pako chaka chimodzi; kuti dziko lingakhale bwinja, ndi zilombo za kuthengo zingakuchulukire. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sindidzaŵapirikitsa chaka chimodzinchimodzi, kuti dzikolo lingadzakhale lopanda anthu ndi kukusiyirani nyama zakuthengo zokhazokha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Komabe sindidzawachotseratu onse mʼchaka chimodzi chifukwa dziko lingadzakhale lopanda anthu ndipo nyama zakuthengo zidzakuchulukirani. |
Ndidzawaingitsa pang'onopang'ono pamaso pako, kufikira utachuluka, ndi kulandira dziko cholowa chako.
Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu chaka chimodzi.
Ndipo Yehova Mulungu wanu adzataya amitundu awa pang'onopang'ono; simuyenera kuwaononga msanga, kuti zingakuchulukireni zilombo.
Koma ana a Yuda sanakhoze kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino.
Ndipo sanaingitse Akanani akukhala mu Gezere; koma Akanani anakhala pakati pa Efuremu, kufikira lero lino, nawaumiriza kugwira ntchito yathangata.