Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa mu ukalamba wake wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wake.
Eksodo 23:26 - Buku Lopatulika M'dziko mwanu simudzakhala wakutaya mwana, kapena wosabala; ndidzakwaniritsa kuwerenga kwa masiku ako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 M'dziko mwanu simudzakhala wakutaya mwana, kapena wosabala; ndidzakwaniritsa kuwerenga kwa masiku ako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Palibe mkazi amene adzapititse padera m'dziko mwanumo, ndipo wosabala sadzaoneka. Ndidzakupatsani moyo wautali. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Palibe mkazi amene adzapite padera kapena kukhala wosabereka mʼdziko mwanu. Ndidzakupatsani moyo wautali. |
Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa mu ukalamba wake wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wake.
Ndipo Isaki anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ake aamuna anamuika iye.
Atakalamba tsono Davide ndi kuchuluka masiku, iye analonga mwana wake Solomoni akhale mfumu ya Israele.
Kuti nkhokwe zathu zidzale, kutipatsa za mitundumitundu; ndi kuti nkhosa zathu ziswane zikwizikwi, inde zikwi khumi kubusako.
Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.
Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.
Sipadzakhalanso khanda la masiku, pena munthu wokalamba osakwanitsa masiku ake; pakuti mwana adzafa wa zaka zana limodzi; ndipo wochimwa pokhala wa zaka zana limodzi adzatemberedwa.
Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoweta zanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.
Muzisunga malemba ake, ndi malamulo ake, amene ndikuuzani lero lino, kuti chikukomereni inu ndi ana anu akukutsatani, ndi kuti masiku anu achuluke padziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu kosatha.
Mudzakhala odalitsika koposa mitundu yonse ya anthu; sipadzakhala mwamuna kapena wamkazi wosabala pakati pa inu, kapena pakati pa zoweta zanu.