Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 23:27 - Buku Lopatulika

27 Ndidzatumiza kuopsa kwanga kukutsogolere, ndipo ndidzapirikitsa anthu onse amene udzafika kwao, ndipo ndidzachita kuti adani ako onse adzakuonetsa m'mbuyo mwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndidzatumiza kuopsa kwanga kukutsogolere, ndipo ndidzapirikitsa anthu onse amene udzafika kwao, ndipo ndidzachita kuti adani ako onse adzakuonetsa m'mbuyo mwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Anthu onse olimbana nanu ndidzaŵachititsa mantha kuti andiwope Ine. Ndidzadzetsa chisokonezo pakati pa anthu amene mukumenyana nawo. Ndipo adani anu onse ndidzaŵathamangitsa liŵiro lamtondowadooka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 “Ine ndidzawachititsa mantha ndi kusokoneza anthu onse amene adzalimbana ndi inu ndipo adani anu onse adzakuthawani.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 23:27
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anapita ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera mizinda yakuwazinga, ndipo sanalondole ana a Yakobo.


Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo, kuti ndiwalikhe akudana ndi ine.


Popeza Ambuye adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magaleta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikulu; nanenana wina ndi mnzake, Taonani mfumu ya Israele watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aejipito, atigwere.


Ndipo anakantha mizinda yonse pozungulira pake pa Gerari; pakuti mantha ochokera kwa Yehova anawagwera; ndipo anafunkha m'mizinda monse, pakuti mudachuluka zofunkha m'menemo.


Ndipo adani anga mwawalozetsa m'mbuyo kwa ine, kuti ndipasule ondidawo.


Pakuti mudzawabweza m'mbuyo, popiringidza m'nsinga zanu pankhope pao.


ndipo ndidzatuma mthenga akutsogolere; ndipo ndidzapirikitsa Akanani, ndi Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;


Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu chaka chimodzi.


Ndipo Mowabu anachita mantha akulu ndi anthuwo, popeza anachuluka; nada mtima Mowabu chifukwa cha ana a Israele.


Yehova adzapirikitsa amitundu awa onse pamaso panu, ndipo mudzalanda amitundu aakulu ndi amphamvu oposa inu.


Palibe munthu adzaima pamaso panu; Yehova Mulungu wanu adzanjenjemeretsa ndi kuopsa dziko lonse mudzapondapo, chifukwa cha inu, monga anenana ndi inu.


Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kuchititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa chifukwa cha iwe.


kuingitsa adani anu onse pamaso panu, monga Yehova adanena.


Koma Yehova Mulungu wanu adzawapereka pamaso panu, nadzawapirikitsa ndi kupirikitsa kwakukulu, kufikira ataonongeka.


Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa