Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 144:13 - Buku Lopatulika

13 Kuti nkhokwe zathu zidzale, kutipatsa za mitundumitundu; ndi kuti nkhosa zathu ziswane zikwizikwi, inde zikwi khumi kubusako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Kuti nkhokwe zathu zidzale, kutipatsa za mitundumitundu; ndi kuti nkhosa zathu ziswane zikwizikwi, inde zikwi khumi kubusako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Nkhokwe zathu zikhale zodzaza, zisunge zokolola za mtundu uliwonse. Nkhosa zathu zibale ana zikwizikwi m'mabusa athu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Nkhokwe zathu zidzakhala zodzaza ndi zokolola za mtundu uliwonse. Nkhosa zathu zidzaswana miyandamiyanda pa mabusa athu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 144:13
10 Mawu Ofanana  

Ndipo mudzadya za sundwe wakale ndi kutulutsa zakale chifukwa cha zatsopano.


Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yotchera mphesa, ndi nyengo yotchera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta nacho chakudya chanu, ndi kukhala m'dziko mwanu okhazikika.


Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.


Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoweta zanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.


Yehova adzakulamulirani dalitso m'nkhokwe zanu, ndi m'zonse mutulutsirako dzanja lanu; ndipo adzakudalitsani m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.


Ndipo anakuchepetsani, nakumvetsani njala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwe, angakhale makolo anu sanawadziwe; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m'kamwa mwa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa