Akachipeza chakubacho chili m'dzanja lake chamoyo, ngakhale ng'ombe, kapena bulu, kapena nkhosa, alipe mowirikiza.
Eksodo 22:7 - Buku Lopatulika Munthu akaikiza ndalama kapena chuma kwa mnansi wake, ndipo zibedwa m'nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe chowirikiza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munthu akaikiza ndalama kapena chuma kwa mnansi wake, ndipo zibeka m'nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe chowirikiza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Munthu akasungiza mnzake ndalama kapena zina zamtengowapatali, ndipo zibedwa m'nyumba mwa munthumo, mbalayo ilipire moŵirikiza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ngati munthu asungitsidwa ndi mnzake ndalama kapena katundu, ndipo zinthu zija nʼkubedwa mʼnyumba mwake, wakubayo ngati agwidwa, ayenera kubwezera kawiri chobedwacho. |
Akachipeza chakubacho chili m'dzanja lake chamoyo, ngakhale ng'ombe, kapena bulu, kapena nkhosa, alipe mowirikiza.
Ukayaka moto, nukalandira kuminga, kotero kuti unyeketsa mulu wa tirigu, kapena tirigu wosasenga, kapena munda; woyatsa motoyo alipe ndithu.
Monga mbala ili ndi manyazi pamene igwidwa, chomwecho nyumba ya Israele ili ndi manyazi; iwo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, ndi aneneri ao;
Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zake; mphotho yake ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m'mawa.
Akachimwa munthu nakachita mosakhulupirika pa Yehova nakachita monyenga ndi mnansi wake kunena za choikiza, kapena chikole, kapena chifwamba, kapena anasautsa mnansi wake;
kapena chilichonse analumbirapo monama; achibwezere chonsechi, naonjezepo, limodzi la magawo asanu; apereke ichi kwa mwini wake tsiku lotsutsidwa iye.
Koma ananena ichi si chifukwa analikusamalira osauka, koma chifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoikidwamo.
kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.