Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 22:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “Ngati munthu asungitsidwa ndi mnzake ndalama kapena katundu, ndipo zinthu zija nʼkubedwa mʼnyumba mwake, wakubayo ngati agwidwa, ayenera kubwezera kawiri chobedwacho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 Munthu akaikiza ndalama kapena chuma kwa mnansi wake, ndipo zibedwa m'nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe chowirikiza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Munthu akaikiza ndalama kapena chuma kwa mnansi wake, ndipo zibeka m'nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe chowirikiza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 “Munthu akasungiza mnzake ndalama kapena zina zamtengowapatali, ndipo zibedwa m'nyumba mwa munthumo, mbalayo ilipire moŵirikiza.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 22:7
10 Mawu Ofanana  

“Ngati chiweto chobedwacho chipezeka chamoyo mʼmanja mwake, kaya ndi ngʼombe kapena bulu kapena nkhosa, mbalayo ibwezere ziweto ziwiri pa chiweto chobedwacho.


“Ngati munthu ayatsa moto, motowo ndikukafika mpaka ku munda ndi kuwotcha mulu wa tirigu kapena tirigu wosadula, kapena munda wonse, ndiye kuti munthu amene anayatsa motoyo alipire.


“Monga momwe mbala imachitira manyazi pamene yagwidwa, moteronso nyumba ya Israeli idzachita manyazi; Aisraeliwo, mafumu ndi akuluakulu awo, ansembe ndi aneneri awo.


“ ‘Musapsinje mnzanu kapena kumulanda zinthu zake. “ ‘Musasunge malipiro a munthu wantchito usiku wonse mpaka mmawa.


Yehova anawuza Mose kuti,


“Ngati munthu wina aliyense achimwa, nachita zinthu mosakhulupirika kwa Yehova chifukwa cha kunyenga mnzake pokana kumubwezera zimene anamusungitsa, kapena kumubera kapenanso kumulanda,


kapena zimene analumbira monyengazo. Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, iye ayenera kumubwezera mwini wake zinthu zonsezi ndi kuwonjezerapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse.


Iye sananene izi chifukwa cha kuganizira osauka koma chifukwa anali mbava; ngati wosunga thumba la ndalama, amabamo zomwe ankayikamo.


kapena akuba, kapena aumbombo, kapena oledzera, kapena achipongwe, kapena opeza ndalama mwachinyengo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa