Ndipo mdzakazi wanu ndinali nao ana aamuna awiri, ndipo awiriwo analimbana kumunda, panalibe wina wakuwaletsa, koma wina anakantha mnzake namupha.
Eksodo 21:18 - Buku Lopatulika Akalimbana amuna, ndipo wina akakantha mnzake ndi mwala, kapena ndi nkhonya, wosafa iye, koma wakhulungira pakama; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akalimbana amuna, ndipo wina akakantha mnzake ndi mwala, kapena ndi nkhonya, wosafa iye, koma wakhulungira pakama; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Anthu akamenyana, ndipo wina mwa iwowo amenya mnzake ndi mwala kapena nkhonya, koma osamupha mnzakeyo, munthu womenyedwayo akadwala nakagona pa bedi, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ngati anthu awiri akangana ndipo wina amenya mnzake ndi mwala kapena nkhonya koma wosamupha, womenyedwayo akadwala nagona pa bedi, |
Ndipo mdzakazi wanu ndinali nao ana aamuna awiri, ndipo awiriwo analimbana kumunda, panalibe wina wakuwaletsa, koma wina anakantha mnzake namupha.
M'mawa mwake anatulukanso, ndipo, taonani, anthu awiri Ahebri alikumenyana; ndipo ananena ndi wochimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako?
akaukanso, nakayendayenda pabwalo ndi ndodo yake, womkanthayo azikhala womasuka; pakutsotsa pake pokha azimbwezera, namchizitse konse.
Munthu akakantha mnyamata wake, kapena mdzakazi wake, ndi ndodo, ndipo akafa padzanja pake; ameneyo alangidwe ndithu.
Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kuphwetekwa; alipe ndithu, monga momwe amtchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oweruza.
Akalimbana wina ndi mnzake, nakayandikiza mkazi wa winayo kulanditsa mwamuna wake m'dzanja la wompandayo, nakatulutsa dzanja lake, ndi kumgwira kudzivalo;