Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 21:20 - Buku Lopatulika

20 Munthu akakantha mnyamata wake, kapena mdzakazi wake, ndi ndodo, ndipo akafa padzanja pake; ameneyo alangidwe ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Munthu akakantha mnyamata wake, kapena mdzakazi wake, ndi ndodo, ndipo akafa padzanja pake; ameneyo aliridwe ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 “Munthu akamenya kapolo wake wamwamuna kapena wamkazi ndi ndodo, ndipo kapoloyo afera pomwepo, munthuyo adzalangidwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 “Ngati munthu amenya kapolo wake wamwamuna kapena mdzakazi ndi ndodo, kapolo uja ndikufa chifukwa cha kumenyedwako, munthuyo ayenera kulangidwa.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 21:20
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa iye, Chifukwa chake aliyense amene adzapha Kaini kudzabwezedwa kwa iye kasanu ndi kawiri. Ndipo Yehova anaika chizindikiro pa Kaini, kuti asamuphe aliyense akampeza.


Ngati Kaini adzabwezeredwa kasanu ndi kawiri, koma Lameki makumi asanu ndi awiri.


Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m'chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu.


akaukanso, nakayendayenda pabwalo ndi ndodo yake, womkanthayo azikhala womasuka; pakutsotsa pake pokha azimbwezera, namchizitse konse.


Koma akakhala wosafa tsiku limodzi kapena awiri, asalangike, pakuti ndiye ndalama ya mbuye wake.


Kapolo sangalangizidwe ndi mau, pakuti azindikira koma osavomera.


Wolipsa mwazi mwini wake aphe wakupha munthuyo; pakumpeza amuphe.


pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.


Ndipo diso lanu lisachite chifundo, moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa