ndi kukhululukira anthu anu adachimwira Inu ndi mphulupulu zao zonse adapalamula nazo kwa Inu; ndipo muwachititsire chifundo iwo amene anawagwira ndende, kuti awachitire chifundo;
Eksodo 2:6 - Buku Lopatulika Pamene anakavundukula, anapenya mwanayo; ndipo taonani, khandalo lilikulira. Ndipo anamva naye chifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene anakavundukula, anapenya mwanayo; ndipo taonani, khandalo lilikulira. Ndipo anamva naye chifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atakatsekula kadengu kaja, adapezamo kamwana kakamuna kakungolira. Mtsikanayo adachita nako chifundo kamwanako, ndipo adati, “Kameneka ndi kamwana kachihebri.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye atavundukula anaona mwana wamwamuna akungolira. Iye anamva naye chisoni mwana uja, nati, “Ameneyu ndi mmodzi mwa ana a Chihebri.” |
ndi kukhululukira anthu anu adachimwira Inu ndi mphulupulu zao zonse adapalamula nazo kwa Inu; ndipo muwachititsire chifundo iwo amene anawagwira ndende, kuti awachitire chifundo;
Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.
Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m'mtsinje, koma ana aakazi onse alekeni amoyo.
Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m'mtsinje; ndipo atsikana ake anayendayenda m'mbali mwa mtsinje; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wake akatenge.
Pamenepo mlongo wake ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo?
kuti yense ammasule kapolo wake wamwamuna, ndi wamkazi, pokhala iye Muhebri wamwamuna kapena wamkazi, kuti yense asayese Myuda mnzake kapolo wake;
Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;