Eksodo 2:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Iye atavundukula anaona mwana wamwamuna akungolira. Iye anamva naye chisoni mwana uja, nati, “Ameneyu ndi mmodzi mwa ana a Chihebri.” Onani mutuwoBuku Lopatulika6 Pamene anakavundukula, anapenya mwanayo; ndipo taonani, khandalo lilikulira. Ndipo anamva naye chifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Pamene anakavundukula, anapenya mwanayo; ndipo taonani, khandalo lilikulira. Ndipo anamva naye chifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Atakatsekula kadengu kaja, adapezamo kamwana kakamuna kakungolira. Mtsikanayo adachita nako chifundo kamwanako, ndipo adati, “Kameneka ndi kamwana kachihebri.” Onani mutuwo |
Inu Ambuye tcherani khutu lanu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune ndiponso pemphero la atumiki anu amene amakondwera kuchitira ulemu dzina lanu. Lolani kuti mtumiki wanune zinthu zindiyendere bwino lero ndi kuti mfumu indichitire chifundo.” Nthawi imeneyi nʼkuti ndili woperekera zakumwa kwa mfumu.