Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 2:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m'mtsinje; ndipo atsikana ake anayendayenda m'mbali mwa mtsinje; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wake akatenge.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m'nyanja; ndipo atsikana ake anayendayenda m'mbali mwa nyanja; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wake akatenge.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Nthaŵi ina mwana wamkazi wa Farao adapita kumtsinje komweko kukasamba. Iyeyo anali ndi adzakazi ake, ndipo onsewo ankangoyenda m'mbali mwa mtsinje muja. Tsono mwana wa Farao uja adakaona kadengu kaja m'bangomo, natuma mdzakazi wake kuti akakatenge.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mwana wamkazi wa Farao anapita ku mtsinje wa Nailo kukasamba ndipo adzakazi ake ankayenda mʼmbali mwa mtsinjewo. Tsono mwana wa Farao uja anaona kadenguko pakati pa mabango ndipo anatuma mdzakazi wake kuti akakatenge.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 2:5
12 Mawu Ofanana  

Ndipo makwangwala anamtengera mkate ndi nyama m'mawa, ndi mkate ndi nyama madzulo; namamwa iye mumtsinje.


Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.


Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.


Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.


Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi. Msanje m'nyengo za nsautso;


Pamene anakavundukula, anapenya mwanayo; ndipo taonani, khandalo lilikulira. Ndipo anamva naye chifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri.


Muka kwa Farao m'mawa; taona, atuluka kunka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa mtsinje; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako.


Ndipo Yehova anati kwa Mose Uuke ulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao; taona, atuluka kunka kumadzi; nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, anditumikire.


Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi; aulozetsa komwe afuna.


Koma Yehova anaikiratu chinsomba chachikulu chimeze Yona; ndipo Yona anali m'mimba mwa nsombayi masiku atatu usana ndi usiku.


Pamenepo Yehova analankhula ndi nsombayo, ndipo inamsanzira Yona kumtunda.


ndipo pakutayika iye, anamtola mwana wamkazi wa Farao, namlera akhale mwana wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa