Eksodo 2:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Mwana wamkazi wa Farao anapita ku mtsinje wa Nailo kukasamba ndipo adzakazi ake ankayenda mʼmbali mwa mtsinjewo. Tsono mwana wa Farao uja anaona kadenguko pakati pa mabango ndipo anatuma mdzakazi wake kuti akakatenge. Onani mutuwoBuku Lopatulika5 Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m'mtsinje; ndipo atsikana ake anayendayenda m'mbali mwa mtsinje; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wake akatenge. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m'nyanja; ndipo atsikana ake anayendayenda m'mbali mwa nyanja; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wake akatenge. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Nthaŵi ina mwana wamkazi wa Farao adapita kumtsinje komweko kukasamba. Iyeyo anali ndi adzakazi ake, ndipo onsewo ankangoyenda m'mbali mwa mtsinje muja. Tsono mwana wa Farao uja adakaona kadengu kaja m'bangomo, natuma mdzakazi wake kuti akakatenge. Onani mutuwo |