Ndipo pamene mpongozi wake wa Mose anaona zonsezi iye anawachitira anthu, anati, Chinthu ichi nchiyani uwachitira anthuchi? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala chilili pamaso pako kuyambira m'mawa kufikira madzulo?
Eksodo 18:15 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anati kwa mpongozi wake, Chifukwa anthu amadza kwa ine kudzafunsira Mulungu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anati kwa mpongozi wake, Chifukwa anthu amadza kwa ine kudzafunsira Mulungu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adayankha kuti, “Ndiyenera kuchita zimenezi chifukwa choti anthu amabwera kwa ine, kuti amve zimene Mulungu afuna. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anamuyankha kuti, “Chifukwa anthuwa anabwera kwa ine kudzafunsa zimene Mulungu akufuna. |
Ndipo pamene mpongozi wake wa Mose anaona zonsezi iye anawachitira anthu, anati, Chinthu ichi nchiyani uwachitira anthuchi? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala chilili pamaso pako kuyambira m'mawa kufikira madzulo?
Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoze kuchita Paska tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;
Ndipo atafa Yoswa, ana a Israele anafunsira kwa Yehova ndi kuti, Adzayamba ndani kutikwerera pa Akanani kuwathira nkhondo?