ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;
Eksodo 16:29 - Buku Lopatulika Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, chifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku awiri; khalani yense m'malo mwake munthu asatuluke m'malo mwake tsiku lachisanu ndi chiwiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, chifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku awiri; khalani yense m'malo mwake munthu asatuluke m'malo mwake tsiku lachisanu ndi chiwiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kumbukirani kuti ndine Chauta, amene ndidakupatsani tsiku la Sabata. Tsono chifukwa cha chimenechi ndimakupatsani chakudya chokwanira masiku aŵiri pa tsiku lachisanu ndi chimodzi. Aliyense azingokhala komwe aliriko pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Asachoke ndi mmodzi yemwe pakhomo pake.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Taonani, popeza Yehova wakupatsani Sabata nʼchifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi amakupatsani chakudya cha masiku awiri. Aliyense azikhala pamene ali pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, pasapezeke wotuluka kunja.” |
ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Mukana kusunga zouza zanga ndi malamulo anga kufikira liti?
Koma iwe, lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo chizindikiro pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani.
Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.
pamenepo ndidzauza dalitso langa litsike pa inu chaka chachisanu ndi chimodzi, ndipo chidzapatsa zipatso zofikira zaka zitatu.
Ndipo anapita kwao, nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula monga mwa lamulo.